Competition in this pair is now closed. Discussion and feedback about the competition in this language pair may now be provided by visiting the "Discussion & feedback" page for this pair. Entries may also be individually discussed by clicking the "Discuss" link next to any listed entry. Source text in English A theme of the age, at least in the developed world, is that people crave silence and can find none. The roar of traffic, the ceaseless beep of phones, digital announcements in buses and trains, TV sets blaring even in empty offices, are an endless battery and distraction. The human race is exhausting itself with noise and longs for its opposite—whether in the wilds, on the wide ocean or in some retreat dedicated to stillness and concentration. Alain Corbin, a history professor, writes from his refuge in the Sorbonne, and Erling Kagge, a Norwegian explorer, from his memories of the wastes of Antarctica, where both have tried to escape.
And yet, as Mr Corbin points out in "A History of Silence", there is probably no more noise than there used to be. Before pneumatic tyres, city streets were full of the deafening clang of metal-rimmed wheels and horseshoes on stone. Before voluntary isolation on mobile phones, buses and trains rang with conversation. Newspaper-sellers did not leave their wares in a mute pile, but advertised them at top volume, as did vendors of cherries, violets and fresh mackerel. The theatre and the opera were a chaos of huzzahs and barracking. Even in the countryside, peasants sang as they drudged. They don’t sing now.
What has changed is not so much the level of noise, which previous centuries also complained about, but the level of distraction, which occupies the space that silence might invade. There looms another paradox, because when it does invade—in the depths of a pine forest, in the naked desert, in a suddenly vacated room—it often proves unnerving rather than welcome. Dread creeps in; the ear instinctively fastens on anything, whether fire-hiss or bird call or susurrus of leaves, that will save it from this unknown emptiness. People want silence, but not that much. | Winning entries could not be determined in this language pair.There were 3 entries submitted in this pair during the submission phase. Not enough votes were submitted by peers for a winning entry to be determined.
Competition in this pair is now closed. | Anthu ambiri masiku ano, makamaka omwe ali m’mayiko otukuka, amafunitsitsa kukhala malo opanda phokoso koma sizitheka. Anthu ambiri amasokonezeka ndi phokoso losatha la magalimoto, kulira kosalekeza kwa mafoni, phokoso la zipangizo zoulutsira mawu zimene zimapezeka m’mabasi komanso mu sitima. Amasokonezekanso ndi phokoso la ma TV omwe amakhala ali wowowowo ngakhalale m’maofesi opanda anthu. Anthu atopa kwambiri ndi phokoso moti akulakalaka malo a phee, opanda phokoso kaya ndi ku nkhalango, pa nyanja, kapenanso malo omwe amakonzedwa mwapadera kuti anthu azikapuma osasokonezedwa ndi chilichonse. Yemwe ananena zimenezi ndi ndi katswiri wa mbiri yakale dzina lake Alain Corbin ndipo anakakhalapo pa univesite ya Paris ku France yomwenso imatchedwa Sorbonne. Iye anakakhala kumeneko pofunafuna malo opanda phokoso. Munthu wina amene ananenanso mfundo yomweyi ndi Erling Kagge, katswiri wofufuza malo wa ku Norway, yemwenso panthawi ina anakakhala Antarctica pofunafuna malo a phee. Komabe, monga mmene Corbin anafotokozera m’buku lake lakuti A History of Silence, masiku ano kulibe phokoso lodetsa nkhawa tikayerekezera ndi mmene zinalili kale. Mwachitsanzo kale kusanabwere matayala a labala, m’misewu munkamveka phokoso logonthetsa la mawilo azitsulo komanso nsapato zosokosera za mahatchi akuponda miyala. Masiku amenewo anthu sankadzipatula n’kumangokhala ndwi pafoni, koma ankacheza n’kumaseka ndi anzawo akakhala m’basi kapena musitima. Mavenda ogulitsa manyuzipepala sankangoziunjika m’milu nkumadikirira koma ankaitanira mokweza kwambiri ngati mmenenso ankachitira mavenda ogulitsa tsabola, maluwa komanso nsomba zaziwisi. M’maholo ochitiramo masewero komanso kumvetsera nyimbo zoimbidwa mwaluso munkamveka phokoso lolulutira, kuseka kapena kuwomba m’manja. Ngakhalenso m’madera akumidzi munkamveka alimi akuimba kwinaku akugwira ntchito zawo zolemetsa. Masiku ano sungamve phokoso ngati limenelo. Chimene chasintha masiku ano sikuchuluka kwa phokoso, limenenso anthu ambiri kale ankadandaula nalo, koma kukula kwa chisokonezo chimene chimabwera chifukwa cha phokosolo. Chisokonezo chimenechi chimachititsa kuti zikhale zovuta kupeza malo opanda phokoso. Komabe palinso nkhawa ina imene imabwera ngati palibiretu phokoso lililonse. Mwachitsanzo munthu amachita mantha kwambiri akhakhala pa malo opandilatu phokoso ngati kunkhalango yamitengo yokhayokha, kuchipululu kopanda anthu kapena akakhala m’nyumba yopanda anthu. Khutu limachita kulakalaka kumva phokoso lililonse, kaya ndi la moto ukuyamba kuyaka, kulira kwa mbalame kapena la kugwa kwa masamba. N’zoona kuti anthu amafuna malo opanda phokoso koma palibe amene angakonde kukhala malo opandilatu phokoso lililonse ngati amenewa. | Entry #22879 — Discuss 0 — Variant: Not specifiednone
Voting points | 1st | 2nd | 3rd |
---|
6 | 1 x4 | 1 x2 | 0 |
| Mutu wa m'badwo, makamaka mu dziko lotukuka, ndikuti anthu amafuna kukhala chete ndipo sangapeze. Kuthamanga kwa magalimoto, njuga zosatha za foni, kulengeza zamakono m'mabasi ndi sitima, wailesi ya kaneme ikuwombera ngakhale maofesi opanda kanthu, ndi batri yosatha ndi zosokoneza. Mtundu wa anthu ukudzikuza wekha ndi phokoso ndipo umalakalaka zosiyana-kaya zakutchire, m'nyanja yaikulu kapena kumalo ena otetezedwa kuti azikhalabe ndi moyo. Alain Corbin, pulofesa wa mbiri yakale, akulemba kuchokera pothawirapo kwake ku Sorbonne, ndi Erling Kagge, wofufuza kafukufuku wa ku Norway, kuchokera kukumbukira za zivomezi za Antarctica, kumene onse ayesa kuthawa. Ndipo komabe, monga Bambo Corbin akunena mu "Mbiri Yokhala chete", mwinamwake palibe phokoso kuposa kale lomwe linalipo. Pamaso pa matayala a nyamakazi, misewu ya mumzinda inali yodzaza ndi makina osungunula a magudumu okhala ndi zitsulo ndi mahatchi pamwala. Musanayambe kudzipatula pafoni pamasom'pamaso, mabasi ndi sitima zinayamba kukambirana. Ogulitsa nyuzipepala sanasiye katundu wawo mulu, koma anawalengeza pamutu waukulu, monga momwe ankagulitsira amalonda a yamatcheri, a violets ndi a mackerel atsopano. Masewera ndi opera anali chisokonezo cha huzzahs ndi kumenyana. Ngakhale kumidzi, amphawi ankaimba pamene ankasokoneza. Iwo samaimba tsopano. Chimene chatsintha sikumveka phokoso, zomwe zaka zapitazi zidakodandaula nazo, koma mlingo wa zododometsa, zomwe zimakhala pamalo omwe chete amatha kuwononga. Kumeneko kumakhala chinthu china chododometsa, chifukwa pamene chimafika-mu kuya kwa nkhalango yamphesa, m'chipululu chamaliseche, mu chipinda chodzidzimutsa-nthawi zambiri chimakhala chosatonthoza osati kulandiridwa. Mantha amawombera; khutu limangoyima pa chirichonse, kaya moto-wake kapena mbalame kuyitana kapena susurrus wa masamba, omwe adzapulumutse ku chisokonezo ichi chosadziwika. Anthu amafuna kukhala chete, koma osati kwambiri | Entry #23776 — Discuss 0 — Variant: Not specifiednone
Voting points | 1st | 2nd | 3rd |
---|
2 | 0 | 0 | 2 x1 |
| Mfundo ya nyengo, makamaka m’maiko otukuka kale, anthu amafunitsitsa pali zii koma ndizosatheka. Pali kulilima kwa zoyenda, kulira mosalekeza kwa mafoni, kutsatsa malonda mwa njira za makono m’mabasi, kapena m’masitima, ma TV akutulutsa phokoso kwambiri m’maofesi m’mene mulibe kanthu kali konse, zonsezi zimabweretsa m’sokonezo mosalekezanso. Mtundu wa anthu ukukhala ndi phokoso koma ufunitsitsa cete – ngakhale mu nkhalango, pa nyanja yotakata kapena pa msonkhano wofunika kukhale cete ndi kuchera khutu. Mkulu wina wa zamaphunziro a mbiri yakale, a profesa Alain Corbin, akulemba kuchokera kwao ku Sorbonne, ndipo a Erling Kagge, nzika ya kudziko la Norway koma katswiri wa zofufuza, mwa kukumbukila bwino kwao za zosasamalirika za ku Antarctica, kumene onse awiriwa anayesa kuthawira. Koma abambo Corbin akutero kuti mu “Mbiri ya Kacetecete”, mulibenso phokoso tsopano koposa m’mene zinalili kale. Kalero pamene kunalibe mathayera odzadza ndi mphweya, makhwalala mu matauni anali odzala ndi phokoso loboola nalo makutu lomwe limacokera ku mawilo ansimbi ndi nsapato za akavalo zikamayenda pa miyala. Anthu asanayambe kudzipatula cifukwa ca ma foni am’manja, mu mabsi ndi mu masitima ankalankhulana. Ogulitsa ma nyunzi-pepala naonso sanagosiya mulu wao nakhala cete ai, koma ankatsatsa mokweza mau, momwemonso anatero ogulitsa zipatso, ndi nsomba zogwidwa kumene. Ku mafiyeta ndi kumalo ena azisudzo ndi koimbira kumeneko ndiye kunali kosaneneka ndi cisawawa ca zoliralira ndipo makani ankacitika mokwezetsa mau. Ngakhale kumalo ena a dziko, anthu osauka ankaimba pomwe anali kugwira nchito yokhetsa nayo thukuta. Koma tsopano saimba ai. Zomwe zasintha sikuti kwenikweni ndi mlingo wa phokoso ai, omwe ngakhale zaka mazana za makedzana ankadandaulapo, cimene casintha ndi mlingo wa cisokonezo, cimene cangotenga malo amene akadangokhala a zii. Palinso coonadi cina, cifukwa ikalowelera – mkatikati mwa nkhalango, ndi m’cipululu copanda zomera, ndi mcipinda cimene okhalamo angocokamo mwadzidzidzi – kawirikawiri zimadetsa mtima koposa kulandiridwa. Mantha amalowamo; khutu lingokhala cicherere pa cina ciriconse, mwina ndi mkokomo wa moto, kapena kulira kwa mbalame kapena ndi mkuntho wa mayani, izi zidzasungika kucitira zakudza zosadziwika. Anthu amafuna cetecete, koma osati kwenikweni ai. | Entry #24200 — Discuss 0 — Variant: Not specifiednone
Voting points | 1st | 2nd | 3rd |
---|
2 | 0 | 1 x2 | 0 |
| | | | | X Sign in to your ProZ.com account... | | | | | | ProZ.com translation contestsProZ.com translation contests offer a fun way to take a break from your normal routine while testing and honing your skills with fellow translators.
ProZ.com Translation Contests. Patent pending. |